Pakati pa ophunzira khumi ndi aŵiriwo, Yudasi Isikarioti anaonedwa kukhala wokhulupirika kotero kuti anapatsidwa ntchito yoŵerengera. Komabe, pamene anaweruza Yesu mogwirizana ndi maganizo ake akuthupi, analephera kulandira chipulumutso. Izi zikutiphunzitsa kuti amene amayesa kumvetsetsa zinthu za Kumwamba, malinga ndi zochitika ndi zizolowezi zomwe adapanga ali padziko lapansi pano, adzalephera kumvetsetsa zinthu zauzimu ndi kulandira chipulumutso.
Monga mmene Yesu, Kristu Ahnsahnghong, ndi Mulungu Amayi anakhazikitsira zitsanzo, pamene tifotokoza choonadi chauzimu m’mawu auzimu ndi kutsatira Mulungu, kunyamula mitanda yathu, tingalandire chipulumutso monga Petro, Yohane, ndi oyera mtima a Mpingo woyambirira.
Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu. Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.
1 Akorinto 2:13–14
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi