Daniele anali pangozi ya kuphedwa chifukwa chopemphera kwa Mulungu. Komabe, iye anadalitsidwa ndi Mulungu kwambiri ndi chikhulupiriro chake chosasunthika ndi choona. Mofanana ndi chitsanzo cha Daniele, Baibulo limanena kuti kulambira sikuyenera kuthetsedwa chifukwa ndi ntchito yopatulika imene anthu a Mulungu ayenera kuyisunga, ndipo ndi njira yosonyezera kuti amalemekeza Mulungu.
Ngati tili ndi chikhulupiriro chotsatira ziphunzitso za m ‘Baibulo, tiyenera kulambira Mulungu pa tsiku lopatulika losankhidwa ndi Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndi malingaliro athu. Mamembala a Mpingo wa Mulungu padziko lonse lapansi amalambira Mulungu molingana ndi Sabata day ndi Zikondwerero Zisanu ndi ziwiri mu Nthawi Zitatu za Pangano Latsopano, zomwe Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi atiphunzitsa.
Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo,
imene olambira oona adzalambira Atate
mumzimu ndi m’choonadi; pakuti Atate
afuna otere akhale olambira ake.
Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira
Iye ayenera kumlambira
mumzimu ndi m’choonadi.
Yohane 4:23-24
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi