Mtumwi Yohane ataona chochitika
zosasangalatsa chimene anthu onse
adzapita kumoto, analira. Komabe,
mmodzi wa akuluwo ananena ndi iye:
“M’tsogolomu, Muzu wa Davide
udzatsegula Baibulo limene lidasindikizidwa
ndi kupulumutsa anthu.” Khristu
Ahnsahnghong anabatizidwa ali ndi
zaka 30, mogwirizana ndi moyo wa
Davide, anamaliza zaka 37 zotsalazo,
ndipo anavumbula pangano latsopano
ndi zinsinsi za Baibulo zimene
zinasindikizidwa, kuphatikizapo choonadi
cha Amayi athu a Kumwamba.
Popeza kuti zinsinsi za m’Baibulo
zikhoza kutsegulidwa ndi Davide yekha,
anthu ayenera kukumana ndi Davide.
Khristu Ahnsahnghong, amene
anabwera ngati Davide, anaphunzitsa
anthu za ufumu wosatha wa
kumwamba, m’malo mwa nkhani za
moyo wosakhalitsa uno. Komanso, Iye
anaphunzitsa kupezeka kwa Mulungu
Amayi, Hava wauzimu, amene anabisika
mkati mwa dongosolo la Mulungu.
Choncho, mayiko onse akukhamukira
ku Mpingo wa Mulungu kumene
Mulungu Amayi amakhala.
Ndipo ndinalira kwambiri, chifukwa
sanapezeke mmodzi woyenera kutsegula
bukulo, kapena kulipenya; ndipo mmodzi
wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona,
Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu
wa Davide, wapambana kuti akhoza
kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu
ndi ziwiri.
Chivumbulutso 5:4-5
Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa
kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro; kotero
Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi
kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera
pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa
iwo amene amlindirira, kufikira
chipulumutso.
Ahebri 9:27-28
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi