Phwando la zipatso zoyamba lokondwerera nthawi ya Mose
mu Chipangano Chakale chinali chithunzithuzi, ndipo Tsiku la Kuuka
kwa akufa m’Chipangano Chatsopano ndiye zenizeni zake.
Yesu Khristu anaukitsidwa m’mawa pa tsiku lotsatira tsiku la Sabata,
Lamulungu, monga chipatso choyamba cha amene anali akugona
kukwaniritsa ulosi wa Phwando la zipatso zoyamba.
Choncho, chifuniro cha Mulungu kuti tisunge Tsiku
la Sabata (Loweruka) monga phwando la sabata iliyonse,
ndi Tsiku la Kuuka kwa akufa ngati phwando la pachaka.
Satana anaika anthu mu khwekhwe la imfa,
kuwapanga iwo kudutsa mu ululu wa imfa;
Komabe, Yesu Khristu anabwera padziko lapansi lino,
kuswa mphamvu ya imfa, ndipo anatsogolera anthu
ku choonadi chotilondolera ku moyo wosatha kudzera pa Tsiku la kuuka kwa akufa.
Masiku ano, mamembala a Mpingo wa Mulungu
samatsatira miyambo yachikunja yogawana mazira,
koma wokudya mkate watsegula maso athu auzimu,
kutsatira chitsanzo cha Yesu Khristu.
Koma tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa,
chipatso choundukula cha iwo akugona . . . .
mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.[1 Akorinto 15:20–22]
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi