Tsiku la kuuka kwa akufa limasonyeza mphamvu yaikulu ya Kristu pogonjetsa mphamvu ya imfa kupyolera pa kuuka kwake kwa akufa, ndipo linakhala maziko a kutsitsimuka kwa Mpingo woyamba. Ndi phwandoso la chimwemwe ndi chiyembekezo chomwe chimatithandiza kusunga chikhulupiriro chathu ngakhale timaponderezedwa kwambiri ndi kuzunzidwa.
Pa Tsiku la Chiukitsiro, Mulungu amapereka chiyembekezo chosangalatsa kuti iwo amene anafa mwa Khristu adzakumana ndi chiukitsiro chokongola ndipo iwo amene ali ndi moyo adzasandulika m’kuntwanima. Ili ndi Tsiku la Kuuka kwa akufa la Pangano Latsopano lomwe limasungidwa molingana ndi ziphunzitso za Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi.
Koma ngati Khristu alalikidwa kuti
waukitsidwa kwa akufa, nanga ena
mwa inu anena bwanji kuti kulibe
kuuka kwa akufa?Koma ngati kulibe
kuuka kwa akufa, Khristunso
sanaukitsidwe;ndipo ngati Khristu
sanaukitsidwe kulalikira kwathu kuli
chabe, chikhulupiriro chanunso chili
chabe.
1 Akorinto 15:12-14
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi