Iwo amene anatenga mawu a Mulungu monga
nthabwala ndipo sanathaŵe anawonongedwa pamene
Mulungu anaweruza dziko lapansi ndi chigumula
m’masiku a Nowa komanso ndi moto m’masiku
a Sodomu ndi Gomora.
Chomwechonso, anthu amene sanakhulupirire mawu a
Yesu akuti, “Pamene mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi
magulu ankhondo, thawani,” koma anagonjetsedwa ndi
lingaliro lachipambano onse anawonongedwa pa kuukira
kwachiŵiri kwa gulu lankhondo la Roma.
Dziko lapansi limatenga chiweruzo chomaliza
cha Mulungu cha moto ngati nthabwala.
Komabe, Mulungu akuyembekezera anthu chifukwa
akufuna kuti aliyense apulumuke kuti asawonongedwe
ngakhale ndi munthu mmodzi yemwe.
Choncho, mamembala a mpingo wa Mulungu
amachitira umboni mwamphamvu ku dziko lonse
lapansi za uthenga wa chipulumutso molingana
ndi chifuniro cha Mulungu.
[N]di kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku
otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda
monga mwa zilakolako za iwo eni,
ndi kunena, Lili kuti lonjezano la
kudza kwake?
. . . m’menemo miyamba potentha moto idzakanganuka,
ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.
Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera
miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo
mukhalitsa chilungamo.
2 Petro 3:3-13
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi