[GAWO1]
Komabe, ndili ku koleji, ndinayamba kuzifunsa
ngati mmene ndinakulira kapena zikhulupiriro za chipembedzo changa zinali zoona
kapena ngati zinali miyambo ndi miyambo chabe.
Chotero pamene ndinali kufunafuna mayankho,
ndinapemphedwa kuphunzira Baibulo ndi mamembala a Mpingo wa Mulungu.
Ndipo pophunzira Baibulo, ndinadabwa kwambiri
ndi zimene anandionetsa m’Baibulo.
Choncho ndinaona kuti zimene Mpingo wa Mulungu unali kuphunzitsa zinali zovomerezeka, ndipo zimenezi n’zoonadi.
[GAWO2]
Pa zinthu zonse zimene ndinaphunzira mu Mpingo wa Mulungu, ndinganene kuti chotsegula maso kwambiri ndiponso chokhudza mtima kwambiri kwa ine chinali kuphunzira za Mulungu Amayi.
Ndipo izo zinali kutitsegula maso chifukwa ife nthawizonse timapita ku tchalitchi ndi kukhulupirira mwa Mulungu Atate, koma pano ndi Baibulo likuchitira umboni za Amayi athu a Kumwamba, Mulungu Amayi.
Ndipo pamene ine ndinaphunzira za Yerusalemu Watsopano, Mkwatibwi, mkazi wa mwanawankhosa anali Amayi athu a Kumwamba, ine ndinadabwa kumva kuti Iwo anachitiridwa umboni kuyambira kuchiyambi kwa Buku la Genesis, pamene Mulungu anati, “Tipange munthu mchifanizo chathu monga mwa chikhalidwe chathu.”
Kotero apa inu munali ndi izi.
Munali ndi Mulungu Amayi ochitiridwa umboni kuchokera m’buku loyamba la Genesis mpaka bukhu lomalizira la Chivumbulutso.
Ndipo ndinazindikira kuti umboni wa Mulungu Amayi unachokera kuchiyambi cha Baibulo.
Izi zili paliponse m'malemba onse.
[GAWO3]
Kukhulupirira Mulungu Amayi kwa ine kunali kosavuta pamene ndinaphunzira Baibulo,
komabe, kunali kovuta pang’ono kukhulupirira kuti Mulungu Amayi anabwera m’thupi.
Ndipo ndikuganiza kuti njira yomwe ndinatha kumvetsetsa pomaliza pake inali poyang'ana mmbuyo ku zomwe zinachitika zaka 2,000 zapitazo ndi Yesu.
Ndipo kupyolera mu zimenezo, ndinatha kuzindikira kuti, kuti ndilandire Amayi Akumwamba amene anabwera m’thupi, sindiyenera kuyandikira kapena kukhulupirira Mulungu Amayi kudzelera m’kaganizidwe kanga kakang’ono, malingaliro, kapena kupenekera chabe.
Ndipo ndiyenera kuona ndi kukhulupirira Amayi a Kumwamba kudzera mu maulosi a m’Baibulo.
[GAWO 4]
Ngati pali ena amene amavutika kuvomereza Mulungu Amayi, ndingawauwuze kuti ayambe kumvetsetsa Mulungu Amayi poyang'ana chilengedwe chowazungulira.
Moyo ukuchokera kwa amayi, ndilo lamulo la Mulungu losasinthika la chilengedwe limene Iye mwini anakonza.
Ndipo chifukwa chake ndi chakuti Mulungu ankafuna kutisonyeza ife kuti sipalibe Atate okha komanso pali Amayi amene amatipatsa ife moyo wosatha.
[GAWO5]
Ndisanabwere ku Mpingo wa Mulungu, ndinali ndi nkhawa nthawi zonse ngati ndingapange zisankho zoyenera m'moyo, komanso ngati ndingakhale ndi moyo wabwino kapena ayi.
Komabe, nditalandira chowonadi ndi kuphunzira za malamulo a Mulungu, pomalizira pake ndinadzimva kukhala wodzidalira ndi wokondwa ndi mtendere kuti ndikhoza kumvera Mulungu ndi kukhala ndi moyo woyenera monga mwana wa Mulungu ndi kulowa Kumwamba.
Ngati pali aliyense amene akuganiza zobwera ku Mpingo wa Mulungu, ndingakulimbikitseni kuti muzibwera nthawi iliyonse yomwe muli ndi mwayi wophunzira Baibulo.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi