Mulungu anapatsa anthu onse nthawi yolapa machimo awo amene anachita Kumwamba komanso mwayi wokhulupirira Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi amene anabwera m’thupi. Pambuyo pake, molingana ndi ntchito za munthu aliyense, Mulungu adzalekanitsa iwo amene adzapita Kumwamba ndi amene adzaweruzidwa.
Pakati pa amene adzaweruzidwe, pali amuna onga Yudasi Isikariote amene anagulitsa Yesu pa chiweruzo cholakwika, ndi aneneri onyenga onga Balaamu amene anaingitsa anthu a Mulungu m’kulambira mafano ndi uphungu wake woipa, ndiponso anthu amene anawononga choonadi cha Mulungu ndi kulambira mulungu dzuŵa kudzera mu malamulo monga kupemphera Sunday ndi Khrisimasi monga momwe Mfumu Ahabu ndi Yezebeli adatengera munda wa mpesa wa Naboti.
Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova.
Numeri 31:16
Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.
Chivumbulutso 2:14
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi