Gehena ndi malo owopsa kwambiri, kumene ndikovuta kulandira angakhale dontho la madzi pamene uli m'mazunzo a moto. (Luka 16:24)
Yesu anati ngati dzanja lathu, phazi, kapena diso litichimwitsa, ndi bwino kulidula kapena kulikolowola, kusiyana ndi kupita ku gehena. (Marko 9:43)
Ndichifukwa chakuti mazunzo a gehena sangayerekezedwe ndi ululu wodula chiwalo cha thupi lathu.
"Kumene mphutsi yawo siifa, ndi moto suzima ku gehena." (Marko 9:48)
“Pakuti onse adzathiridwa mchere wamoto” (Marko 9:49)
Ngakhale chilango cha gehena ndi chopweteka kwambiri, sitingathe kufa mwatokha.
Ku gehena, kulibe chisangalalo cha moyo, kulibe mpumulo, kapena chiyembekezo cha chipulumutso, koma ululu, madandaulo ndi chisoni chokha.
Chifukwa chiyani timapita ku gehena ngati sitilapa titamva uthenga wabwino?
Tisanabadwe padziko lapansi, tinali angelokumwamba. (Yobu 38:4–21)
Komabe, tinachimwa kumwamba ndikulandira chilango chopita ku gehena. Choncho tinabadwa pa dziko,ndende yauzimu, ndipo tili kuno moyembekedzera. (Ezekiele28:13–17)
Ngati sitifunafuna njira yopewera chilango cha gehena padziko lino, tsogolo lathu ndilopita ku gehena latsimikizidwa.
“Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi la imfa iyi?” (Aroma 7:24)
Mulungu anachitira chifundo anthu omwe anayenera kulandira chilango cha gehena, ndipo Iye Mwini anabwera padziko kusonyeza njira yopewera chilango cha gehena.
“Ndadza kudzaitana ochimwa kuti alape.” (Luka 5:32)
Kuti atikhululukire machimo athu otsogolera kuimfa ndi kutipulumutsa ku chilango cha gehena, Mulungu anapereka thupi ndi mwazi Wake ngati dipopa anthu, ochimwa.
“Tengani, idyani; mkate wa Paska ndi thupi langa.” (Mateyu 26:26)
“Vinyo wa Paska ndi mwazi Wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.” (Mateyu 26:28)
Tikasunga Paska wa pangano latsopano, timadalitsidwa ndi chikhululukiro cha machimo ndi kupulumutsidwa ku chilango cha gehena.
Ndiponso, tikhoza kulandira moyo wosatha ndikubwerera kumwamba.
“Iyewakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.” (Yohane 6:54)
Komabe, ngati tikana uthenga wakuti, “Landirani chikhululukiro cha machimo ndi moyo wosatha kudzera mu Paska,”
machimo amene tinachita kumwamba sangakhululukidwe, ndipo tidzalandira chilango cha gehena monga momwe zinakonzedwera.
“Ndinalakalaka ndithu kudya Paska uwu pamodzi ndinu ndisanayambe kusautsidwa.” (Luka 22:15)
Chonde sungani Paska wa pangano latsopano, chizindikiro cha Mulungu pa chikhululukiro cha machimo, ndikubwerera kumwamba!
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi