Dziko lonse lapansi limakondwerera kubadwa kwa Yesu pa Khrisimasi (Dis. 25). Komabe, tsiku lakubadwa kwa Yesu mulibemo mu Baibulo. Limanena kuti abusa amene anali kuyang’anira nkhosa zawo kuthengo, anatamanda Yesu. ( Luk 2:8 )
Sizingatheke kuyang’anira nkhosa kuthengo m’nyengo yozizira. Kodi Yesu anabadwadi pa Dis. 25? Akhristu oyambirira sanakondwelereko kubadwa kwa Yesu.
Ndiye, kodi Khirisimasi inachokera kuti? Disembala 25, Khirisimasi . . .
“Disembala 25 SI tsiku lakubadwa kwa Yesu, koma la mulungu wa dzuwa.
Khirisimasi inachokera ku chikondwerero chachikunja cha dzuwa losagonjetseka.”[Encyclopedia Britannica]
‘Chani? Khirisimasi inachokera ku chikondwerero chachikunja?’
“Ku Roma wakale, kunali phwando lotchedwa Saturnalia kuyambira pa Disembala 17 mpaka 24.”[Mbiri ya mpingo yachikhristu]
“Pachikondwererochi, anthu ankangosangalala mosasamala kanthu za chuma kapena udindo.” [Mbiri ya mpingo Yachikhristu]
‘Ayi! Zinatheka bwanji!!! Khrisimasi, Dis. 25, si tsiku la kubadwa kwa Yesu!!!’
“Dis. 25, pamene masiku amapita chisogolo, inatengedwa kukhala tsiku la kubadwa kwa mulungu Mithra.”[Encyclopedia Britannica]
Pachifukwa cha kuponderedza chikhulupiriro cha Mithra, Tchalitchi cha Katolika wa Chiroma chinakondwerera pwandoli pa kusintha “tsiku la kubadwa kwa mulungu dzuŵa” kukhala tsiku la kubadwa kwa Yesu.[The Golden Bough by James G. Frazer]
Mtengo wa Khirisimasi unachokera ku miyambo yachikunja ya kulambira mitengo.[Encyclopedia Britannica]
Chithunzi cha Santa Claus ndi ndevu zoyera, mu suti yofiira, chinapangidwa mu 1931 chifukwa cha malonda a Coca-Cola.[Illustrated by Haddon Sundblom]
Mipingo imadziŵa bwino lomwe kuti Khrisimasi si tsiku la kubadwa kwa Yesu.
Komabe, amanama kuti Khrisimasi ndi tsikulakubadwa kwa Yesu.
Akhristu ali mumdima wandiweyani pankhani imeneyi.
“Panali mu AD 354 pamene Khrisimasi inakondwereredwa pa Dis.25.”[World Book Encyclopedia]
Pambuyo pa AD 354? Ophunzira ndi atumwi a Yesu sanakondwere nawo Khirisimasi!
“Khirisimasi sinakhazikitsidwe ndi Mulungu, kapena kuikidwa mu Baibulo.”[Cyclopedia of Biblical, Theological and Ecclesiastical Literature]
Iwo anasintha tsiku la kubadwa kwa mulungu dzuŵa kukhala tsiku la kubadwa kwa Yesu!
Izi ndizowopsa! Baibulo limanena kuti ngati anthu asunga malamulo opangidwa ndi anthu, amalambira Mulungu pachabe. (Mat 15:9)
Zinalembedwa m’Baibulo kambirimbiri kuti Aisrayeli anawonongedwa chifukwa chotsatira miyambo yachikunja! (Ezekieli 11:8-12) M’chipululu cha Sinai, iwo ankaganiza kuti akulambira Yehova Mulungu koma ankalambira fano. (Eks 32:1-6)
Yerobiamu, mfumu ya Kumpoto kwa Israyeli, anachita phwando m’mwezi umene anasankha, ponena kuti amalambira Mulungu. (1Maf 12:25-33)
Komabe, onse amene analambira mafano anawonongedwa.
Chimodzimodzinso, ngakhale atanena kuti amalambira Yesu pa Khirisimasi, ndi kupembedza mafano chabe. Mapeto a kupembedza mafano ndi chiwonongeko.
Mpingo wa Mulungu wokhazikitsidwa ndi Ahnsahnghong Khristu amene anabwera kachiwiri, sukondwerera Khirisimasi, tsiku lakubadwa kwa mulungu wa dzuwa, limene silipezeka m’Baibulo.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi