Monga mawotchi adapangidwa kuti atilole kuti tiwone nthawi yosawoneka, titha kuwona kudzera m’Baibulo chiweruzo chopita kumwamba kapena gehena m’dziko lauzimu losaoneka.
Popeza Yesu, amene anabwera monga kuunika, anabwera mu dongosolo la Melkizedeki, otsatira ake, mamembala a Mpingo wa Mulungu, nawonso amasunga Paska wa pangano latsopano ndi kutsatira ziphunzitso Zake.
Zaka 2,000 zapitazo, anthu anagawanika m’magulu awiri—iwo amene anakhulupirira Yesu amene anabwera m’thupi monga Mpulumutsi wawo ndi iwo amene sanakhulupirire, ndipo mu m’badwo wa Mzimu Woyera, pali iwo amene anakhulupirira Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, amene anabwera monga Mzimu ndi Mkwatibwi, ndi iwo amene sanatero.
Baibulo limanena kuti chiweruzo cha Mulungu chatsimikiziridwa kale, kutengera chikhulupiriro ichi.
Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa.
Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.
Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.
Yohane 3:19-21
Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.
1 Yohane 1:5
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi