Pamene Yesu, Mulungu Wamphamvuyonse, anabwera m ‘thupi kuti apulumutse anthu, anthu ambiri anamunyoza.
Komabe, panali anthu amene analemekeza Iye monga mkazi amene anathira mafuta onunkhira pamutu pa Yesu, Kenturiyo, mkazi amene amavutika ndi kutaya magazi, ndi Zakeyu.
Oyera mtima a Mpingo woyamba analandira Yesu ndi chikhulupiriro chotero, ndipo m’ malo mwake, analandira mphatso ya Mzimu Woyera wa chisomo.
Mamembala a Mpingo wa Mulungu amakhulupirira kuti Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi ndi Apulumutsi amene anabwera malinga ndi ulosi, “Mulungu adzabwera ngati Mzimu ndi Mkwatibwi mu m’badwo wa Mzimu Woyera,” ndi kuwalemekeza.
Mulungu amawapatsa Mzimu Woyera wa mvula yotsiridza, yayikulu kuposa ya Mpingo woyambirira, yomwe imatsogolera ku ntchito yodabwitsa ya anthu kuchitira umboni za Mulungu padziko lonse lapansi.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi