Pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo, poyamba Mulungu anaulula mphamvu ya Paska, ndipo analengeza za Paska kudzera m’Chilamulo cha Mose, kuwalamula kuti azisunga kwa mibadwo ili mkudza pa nthawi yoikidwiratu. Pambuyo pake, anthu a Mulungu adatamandidwa ndi kutetezedwa ku matsoka atasunga Paska, ndipo Yesu adasunganso Paska ndi ophunzira ake, kuwapatsa madalitso a moyo wosatha.
Popeza Paska inathetsedwa mu 325 AD, mipingo yonse yakhala ikutsatira miyambo ya mulungu wachikunja. Komabe, mamembala a Mpingo wa Mulungu anazindikira kufunikira kwa Paska, yomwe Mulungu adalamula anthu Ake kuti azikondwerera m’mibadwo yomwe ili mkudza, kudzera m’ziphunzitso za Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi, ndikuzisunga.
Ndipo mfumu inalamulira anthu
onse, kuti, Mchitireni Yehova
Mulungu wanu Paska, monga
mulembedwa m’buku ili la
chipangano. . . . Ndipo asanabadwe
iye panalibe mfumu wolingana naye,
imene inatembenukira kwa Yehova
ndi mtima wake wonse, ndi moyo
wake wonse, ndi mphamvu yake
yonse, monga mwa chilamulo
chonse cha Mose; atafa iyeyu
sanaukenso wina wolingana naye.
2 Mafumu 23:21–25
Nati Iye, Mukani kumzinda kwa
munthu wina wake, mukati kwa
Iye, Mphunzitsi anena, Nthawi
yanga yayandikira; ndidzadya
Paska kwanu pamodzi ndi
ophunzira anga.Ndipo
ophunzira anachita monga
Yesu anawauza, nakonza Paska.
Mateyu 26:18–19
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi