Anthu amaganiza kuti mapeto a moyo wawo padziko lapansi pano ndi mapeto a chirichonse, koma kumwamba ndi gehena zilipo, ndipo pamene moyo wawo mu dziko langodya zitatu kutha, iwo onse adzabwerera ku dziko lawo loyambirira. Yesu ananyamula machimo a anthu pamtanda ndipo anakhazikitsa pangano latsopano kuti atenge ana ake okondedwa kupita kumwamba, osati ku gehena, malo a chilango.
Gehena, monga momwe zafotokozeredwa m’Baibulo, ndi malo ovutika kwambiri. Ichi ndichifukwa chake Khristu Ahnsahnghong ndi Mulungu Amayi adadziwikanso pangano latsopano, ndikupatsa anthu mwayi wosangalala ndi ulemerero wamuyaya mu ufumu wakumwamba.
Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro . . . Ahebri 9:27
Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m’nyanja ya moto ndi sulufure , kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi. ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake . . . Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa m’nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto. Chivumbulutso 20:10–14
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi